Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 5:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali tsiku lacitatu, Estere anabvala zobvala zace zacifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wace wacifumu m'nyumba yacifumu, pandunji polowera m'nyumba.

2. Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuruyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yacifumu yagolidi inali m'dzanja lace. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo.

3. Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkuru? pempho lanu nciani? lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.

4. Ndipo Estere anati, Cikakomera mfumu, adze mfumu ndi Hamani lero ku madyerero ndinawakonzera.

5. Niti mfumu, Mumfulumize Hamani, acitike mau a Estere. Nidza mfumu ndi Hamani ku madyerero adawakonzera Estere.

Werengani mutu wathunthu Estere 5