Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 9:23-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Pamenepo Mose anasamulira ndodo yace kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anabvumbitsa matalala pa dziko la Aigupto.

24. Potero panali matalala, ndi mota wakutsikatsika pakati pa matalala, coopsa ndithu; panalibe cotere m'dziko lonse la Aigupto ciyambire mtundu wao.

25. Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Aigupto zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo.

26. M'dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israyeli, munalibe matalala.

27. Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndacimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa,

28. Pembani kwa Yehova; cifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso.

29. Ndipo Mose ananena naye, Poturuka m'mudzi ine, ndidzasasatulira manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.

30. Koma inu ndi anyamata anu ndidziwa kuti simudzayamba kuopa nkhope ya Yehova Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 9