1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkuru wako adzakhala mneneri wako.
2. Iwe uzdankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkuru wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.
3. Koma Ine ndidzaumitsa mtima wace wa Farao, ndipo ndidzacurukitsa zizindikilo ndi zozizwa zanga m'dziko la Aigupto.