Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 40:26-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo anaika guwa la nsembe lagolidi m'cihema cokomanako cakuno ca nsaru yocinga;

27. nafukizapo cofukiza ca pfungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose.

28. Ndipo anapacika kukacisi nsaru yotsekera pakhomo.

29. Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la kacisi wa cihema cokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.

30. Ndipo anaika mkhate pakati pa cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba.

31. Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ace amuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m'menemo;

32. pakulowa iwo m'cihema cokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.

33. Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa cihema ndi guwa la nsembe, napacika nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza nchitoyi.

34. Pamenepo mtambo unaphimba cihema cokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kacisiyo.

35. Ndipo Mose sanathe kulowa m'cihema cokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kacisi.

36. Ndipo pakukwera mtambo kucokera kukacisi, ana a Israyeli amayenda maulendo ao onse;

37. koma ukapanda kukwera mtambo, samayenda ulendo wao kufikira tsiku loti wakwera.

38. Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pakacisi msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israyeli, m'maulendo ao onse.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 40