Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 40:19-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo anayalika hema pamwamba pa kacisi, naika cophimba ca cihema pamwamba pace; monga Yehova adamuuza Mose.

20. Ndipo anatenga mboniyo, naiika mlikasa, napisa mphiko palikasa, naika cotetezerapo pamwamba pa likasa;

21. nalowa nalo likasa m'kacisi, napacika nsaru yocinga, nacinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.

22. Ndipo anaika gomelo m'cihema cokomanako, pa mbali ya kumpoto ya kacisi, kunja kwa nsaru yocinga.

23. Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

24. Ndipo anaika coikapo nyali m'cihema cokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwela ya kacisi.

25. Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

26. Ndipo anaika guwa la nsembe lagolidi m'cihema cokomanako cakuno ca nsaru yocinga;

27. nafukizapo cofukiza ca pfungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose.

28. Ndipo anapacika kukacisi nsaru yotsekera pakhomo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 40