Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 40:1-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2. Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse kacisi wa cihema cokomanako.

3. Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nucinge likasalo ndi nsaru yocingayo.

4. Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zace; ulongenso coikapo nyalico, ndi kuyatsa nyali zace.

5. Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lazolidi cakuno ca likasa la mboni, numange pakacisi nsaru yotsekera pakhomo.

6. Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la kacisi wa cihema cokomanako.

7. Ukaikenso mkhate pakati pa cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.

8. Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupacika nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo.

9. Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao kacisi, ndi zonse ziri m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zace zonse; ndipo adzakhala wopatulika.

10. Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zace zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulikitsa.

11. Udzozenso mkhate ndi tsinde lace, ndi kuupatula.

12. Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ace amuna ku khomo la cihema cokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi.

13. Nubveke Aroni cobvala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatwa andicitire Ine nchito ya nsembe.

14. Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am'kati;

15. nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andicitire nchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.

16. Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anacita.

17. Ndipo kunali, mwezi woyamba wa caka caciwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa kacisi.

18. Ndipo Mose anautsa kacisi, nakhazika makamwa ace, naimika matabwa ace, namangapo mitanda yace, nautsa mizati ndi nsanamira zace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 40