Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 38:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wasitimu; utali wace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, lampwamphwa; ndi msinkhu wace mikono itaru.

2. Ndipo anapanga nyanga zace pa ngondya zace zinai; nyanga zace zinakhala zoturuka m'mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 38