Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 37:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo anapanga coikapo nyali ca golidi woona; mapangidwe ace a coikapo nyalico anacita cosula, tsinde lace ndi thupi lace, zikho zace, mitu yace, ndi maluwa ace zinakhala zocokera m'mwemo;

18. ndi m'mbali zace munaturuka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za coikapo nyali zoturuka m'mbali yace imodzi, ndi mphanda zitatu za coikapo nyali zoturuka m'mbali yace yina;

19. pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi pa mphanda yina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zoturuka m'coikapo nyali.

20. Ndipo pa coikapo nyali comwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yace ndi maluwa ace;

21. ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zoturuka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zoturuka m'mweno, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zoturuka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zocokera m'mwemo.

22. Mitu yao ndi mphanda zao zinaturuka m'mwemo; conseci cinali cosulika pamodzi ca golidi woona.

23. Ndipo anapanga nyali zace zisanu ndi ziwiri ndi mbano zace, ndi zoolera zace, za golidi woona.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 37