1. Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israyeli, nanena nao, Siwa mau amene Yehova anauza, kuti muwacite.
2. Masiku asanu ndi limodzi azigwira nchito; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: ali yense agwira nchito pamenepo, aphedwe,
3. Musamasonkha mota m'nyumba zanu ziri zonse tsiku la Sabata.
4. Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, ndi kuti, Ici ndi cimene Yehova anauza ndi kuti,
5. Mumtengere Yehova copereka ca mwa zanu; ali yense wa mtima womfunitsa mwini abwere naco, ndico copereka ca Yehova;
6. golidi, ndi siliva, ndi mkuwa; ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;
7. ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wasitimu;
8. ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi cofukiza ca pfungo lokoma;