Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 34:27-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israyeli.

28. Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadya mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.

29. Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lace la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwa kuti khungu la nkhope yace linanyezimira popeza iye adalankhula naye.

30. Ndipo pamene Aroni ndi ana onse a Israyeli anaona Mose, taonani, khungu la nkhope yace linanyezimira; ndipo anaopa kumyandikiza.

31. Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao.

32. Ndipo atatero, ana onse a Israyeli anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m'phiri la Sinai.

33. Ndipo Mose atatha kulankhula nao, anaika cophimba pankhope pace.

34. Koma pakulowa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi iye, ariacotsa cophimbaco, kufikira akaturuka; ndipo ataturuka analankhula ndi ana a Israyeli cimene adamuuza.

35. Ndipo ana a Israyeli anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso cophimba pankhope pace, kufikira akalowa kulankhula ndi iye.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 34