Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 34:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa.

2. Nukonzekeretu m'mawa, nukwere m'mawa m'phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba pa phiri.

3. Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu ali yense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikuru zisadye kuphiri kuno.

4. Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m'phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m'dzanja mwace magome awiri amiyala.

5. Ndipo Yehova anatsika mumtambo, naimapo pamodzi ndi iye, napfuula dzina la Yehova.

6. Ndipo Yehova anapita pamaso pace, napfuula, Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wocuruka, ndi wacoonadi;

7. wakusungira anthu osawerengeka cifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kucimwa; koma wosamasula woparamula; wakulangira ana ndi zidzukulu cifukwa ca mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai.

8. Ndipo Mose anafulumira, naweramira pansi, nalambira.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 34