Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 31:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Za amisiri opanga nchitoyi, Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2. Taona ndaitana ndi kumchula dzina lace, Bezaleli, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuke la Yuda;

3. ndipo ndamdzaza nd mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi cidziwitso, ndi m'nchito ziri zonse,

4. kulingirira nchito zaluso, kucita ndi golidi ndi siliva ndi mkuwa,

5. ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kuzokota mtengo, kucita nchito ziri zonse.

6. Ndipo Ine, taona, ndampatsa Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m'mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe;

7. cihema cokomanako, likasa la mboni, ndi cotetezerapo ciri pamwamba pace, ndi zipangizo zonse za cihemaco;

8. ndi gomelo ndi zipangizo zace, ndi coikapo nyali coona ndi zipangizo zace, ndi guwa la nsembe lofukizapo;

9. ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate ndi tsinde lace;

10. ndi zobvala zotumikira nazo, ndi zobvala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, zakucita nazo nchito ya nsembe;

Werengani mutu wathunthu Eksodo 31