Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 30:29-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.

30. Ndipo udzoze Aroni ndi ana ace amuna, ndi kuwapatula andicitire nchito ya nsembe.

31. Nulankhule ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu.

32. Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ace; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.

33. Ali yense amene akonza ena otere, kapena ali yense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wace.

34. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi libano loona; miyeso yofanana;

35. ndipo uzikonza nazo cofukiza, cosanganiza mwa macitidwe a wosanganiza, cokometsera ndi mcere, coona, copatulika;

36. nupere cina cisalale, nuciike cakuno ca mboni m'cihema cokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uciyese copatulika ndithu.

37. Koma za cofukizaco ucikonze, musadzikonzere nokha cina, mwa makonzedwe ace amene; muciyese copatulika ca Yehova.

38. Ali yense wokonza cina cotere kununkhizapo, asadzidwe kwa anthu a mtundu wace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 30