Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 30:23-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu, ndi kinimani lonunkhira limodzi mwa magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi kane lonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,

24. ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi;

25. ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa macitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika.

26. Ndipo udzoze nao cihema cokomanako, ndi likasa la mboni,

27. ndi gomelo ndi zipangizo zace zonse, ndi coikapo nyali ndi zipangizo zace,

28. ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lace.

29. Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.

30. Ndipo udzoze Aroni ndi ana ace amuna, ndi kuwapatula andicitire nchito ya nsembe.

31. Nulankhule ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu.

32. Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ace; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.

33. Ali yense amene akonza ena otere, kapena ali yense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wace.

34. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi libano loona; miyeso yofanana;

35. ndipo uzikonza nazo cofukiza, cosanganiza mwa macitidwe a wosanganiza, cokometsera ndi mcere, coona, copatulika;

36. nupere cina cisalale, nuciike cakuno ca mboni m'cihema cokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uciyese copatulika ndithu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 30