Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 30:18-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa ciliema cokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.

19. Ndipo Aroni ndi ana ace amuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao;

20. pakulowa iwo m'cihema cokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova;

21. asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zace, mwa mibadwo yao.

22. Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti,

23. Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu, ndi kinimani lonunkhira limodzi mwa magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi kane lonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,

24. ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi;

25. ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa macitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika.

26. Ndipo udzoze nao cihema cokomanako, ndi likasa la mboni,

27. ndi gomelo ndi zipangizo zace zonse, ndi coikapo nyali ndi zipangizo zace,

28. ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zace zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 30