Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 30:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ici acipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo copereka ca Yehova.

14. Yense wakupita kwa owerengedwawo, wa zaka makumi awiri ndi wa mphambu zace, apereke coperekaco kwa Yehova.

15. Wacuma asacurukitsepo, ndi osauka asacepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka copereka kwa Yehova, kucita coteteza ca miyoyo yanu.

16. Ndipo uzilandira ndarama za coteteza kwa ana a Israyeli, ndi kuzipereka pa nchito ya cihema cokomanako; kuti zikhale cikumbutso ca ana a Israyeli pamaso pa Yehova, kucita coteteza ca miyoyo yanu.

17. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti,

18. Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa ciliema cokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 30