Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 28:14-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. ndi maunyolo awiri a golidi woona; uwapote ngati zingwe, nchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.

15. Upangenso capacifuwa ca ciweruzo, nchito ya mmisiri; uciombe mwa ciombedwe ca efodi; uciombe ndi golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

16. Cikhale campwamphwa, copindika, utali wace cikhato cimodzi, ndi kupingasa kwace cikhato cimodzi.

17. Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba;

18. ndi mzere waciwiri wa nofeki, safiri, ndi yahaloni;

19. ndi mizere wacitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama;

20. ndi mzere wacinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golidi m'zoikamo zao.

21. Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israyeli, khumindiawiri, monga maina ao; monga malocedwe a cosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 28