Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 25:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Monga mwa zonse Ine ndirikuonetsa iwe, cifaniziro ca kacisi, ndi cifaniziro ca zipangizo zace zonse, momwemo ucimange.

10. Ndipo azipanga likasa la mtengo wasitimu: utali wace mikono iwiri ndi hafu, kupingasa kwace mkono ndi hafu, msinkhu wace mkono ndi hafu.

11. Ndipo ulikute ndi golidi woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolidi pozungulira pace.

12. Ndipo uliyengere mphete zinai zagolidi, ndi kuziika ku miyendo yace inai; mphete ziwiri pa mbali yace yina, ndi mphete ziwiri pa yina.

13. Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi.

14. Nupise mphiko m'mphetezo pa mbali zace za likasa, zakunyamulira nazo likasalo.

15. Mphiko zikhale m'zimphete za likasa; asazisolole.

16. Ndipo uziika m'likasamo mboni imene ndidzakupatsa.

17. Ndipo uzipanga cotetezerapo ca golidi woona; utali wace mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwace mkono ndi hafu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 25