Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 25:33-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ku mphanda yina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi ku mphanda inzace zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zoturuka m'coikapo nyalico.

34. Ndipo pa coikapo nyali comwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yace ndi maluwa ace;

35. pakhale mutu pansi pa mphaada ziwiri zoturuka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zoturuka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zoturuka m'mwemo; itere ku mphanda zisanu ndi imodzi zoturuka m'coikapo nyalico.

36. Mitu yao ndi mphanda zao zikhale zoturuka m'mwemo; conseci cikhale cosulika cimodzi ca golidi woona.

37. Ndipo uzipanga nyali zace, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zace, ziwale pandunji pace.

38. Ndipo mbano zace, ndi zoolera zace, zikhale za golidi woona.

39. Acipange ici ndi zipangizo izi zonse za talente wa golidi woona.

40. Ndipo uyang'anire uzipanga monga mwacifaniziro cao, cimene anakuonetsa m'phirimo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 25