Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 25:25-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa cikhato m'kupingasa kwace, ndi pamitanda pace pozungulira upangirepo mkombero wagolidi.

26. Nulipangire mphete zinai zagolidi, ndi kuika mphetezo pa ngondya zinai zokhala pa miyendo yace inai.

27. Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome.

28. Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi, kuti anyamulire nazo gome.

29. Ndipo uzipanga mbale zace, ndi zipande zace, ndi mitsuko yace, ndi zikho zace zakuthira nazo; uzipanga za golidi woona.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 25