Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 25:2-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Lankhula ndi ana a Israyeli, kuti anditengere copereka; ulandire copereka canga kwa munthu ali yense mtima wace umfunitsa mwini.

3. Ndipo coperekaco ucilandire kwa iwo ndi ici: golidi, ndi, siliva, ndi mkuwa,

4. ndi lamadzi, ndi: lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;

5. ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wasitimu;

6. mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za cofukiza ca pfungo lokoma;

7. miyala yaberulo, ndi miyala yoika paefodi, ndi pacapacifuwa.

8. Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao,

9. Monga mwa zonse Ine ndirikuonetsa iwe, cifaniziro ca kacisi, ndi cifaniziro ca zipangizo zace zonse, momwemo ucimange.

10. Ndipo azipanga likasa la mtengo wasitimu: utali wace mikono iwiri ndi hafu, kupingasa kwace mkono ndi hafu, msinkhu wace mkono ndi hafu.

11. Ndipo ulikute ndi golidi woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolidi pozungulira pace.

12. Ndipo uliyengere mphete zinai zagolidi, ndi kuziika ku miyendo yace inai; mphete ziwiri pa mbali yace yina, ndi mphete ziwiri pa yina.

13. Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 25