Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 25:18-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Uzipanganso akerubi awiri agolidi; uwasule mapangidwe ace, pa mathungo ace awiri a cotetezerapo.

19. Nupange kerubi mmodzi ku thungo lino, ndi kerubi wina ku thungo lina; upange akerubi ocokera kucotetezerapo, pa mathungo ace awiri.

20. Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba cotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi ziphenye kucotetezerapo,

21. Ndipo uziika cotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m'likasamo.

22. Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ow kulankhula ndi iwe, ndiri pamwamba pa cotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israyeli.

23. Ndipo uzipanga gome la mtengo wasitimu; utali wace mikono iwiri, ndi kupingasa kwace mkono umodzi, ow msinkhu wace mkono ndi hafu.

24. Ndipo ulikute ndi golidi woona ndi kulipangira mkombero wagolidi pozungulira pace.

25. Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa cikhato m'kupingasa kwace, ndi pamitanda pace pozungulira upangirepo mkombero wagolidi.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 25