10. ndipo anapenya Mulungu wa Israyeli; ndipo pansi pa mapazi ace panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbe.
11. Koma sanaturutsa dzanja lace pa akuru a ena a Israyeli; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa.
12. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi cilamulo ndi malamulo, ndawalembera kuti uwalangize.
13. Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wace; ndipo Mose anakwera m'phiri la Mulungu.
14. Ndipo anati kwa akuru, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa.
15. Ndipo Mose anakwera m'phirimo, ndi mtambo unaphimba phirilo,