Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 21:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituruka waufulu;

6. pamenepo mbuye wace azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wace amboole khutu lace ndi lisungulu; ndipo iye azimgwirira nchito masiku onse.

7. Ndipo munthu akagulitsa mwana wace wamkazi akhale mdzakazi, iyeyo asaturuke monga amaturuka anyamata.

8. Akapanda kumkonda mbuye wace, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu acilendo, popeza wacita naye monyenga.

9. Koma ngati amtomera mwana wace wamwamuna, amcitire monga kuyenera ana akazi.

10. Akamtengera mkazi wina, asacepetse cakudya cace, zobvala zace, ndi za ukwati zace zace.

11. Ndipo akapanda kumcitira izi zitatu, azituruka cabe, osaperekapo ndalama.

12. Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu.

13. Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzace, ndidzakuikirani pothawirapo iye.

14. Koma munthu akacita dala pa mnzace, kumupha monyenga; uzimcotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.

15. Munthuwakukanthaatatewace, kapena amai wace, aphedwe ndithu.

16. Iye wakuba munthu, angakhale wamgulitsa, kapena akampeza m'dzanja lace, aphedwe ndithu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 21