Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 21:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pao.

2. Ukagula mnyamata Mhebri, azigwira nchito zaka zisanu ndi cimodzi; koma cacisanu ndi ciwiri azituruka waufulu cabe.

3. Akalowa ali yekha azituruka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wace azituruka naye.

4. Akampatsa mkazi mbuye wace, ndipo akambalira ana amuna ndi akazi, mkaziyo ndi ana ace azikhala a mbuye wace, ndipo azituruka ali yekha.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 21