1. Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pao.
2. Ukagula mnyamata Mhebri, azigwira nchito zaka zisanu ndi cimodzi; koma cacisanu ndi ciwiri azituruka waufulu cabe.
3. Akalowa ali yekha azituruka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wace azituruka naye.