Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 1:4-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Dani ndi Nafitali, Gadi ndi Aseri.

5. Ndipo amoyo onse amene anaturuka m'cuunomwace mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; kama Yosefe anali m'Aigupto.

6. Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ace onse, ndi mbadwo uwo wonse.

7. Ana a Israyeli ndipo anaswana, nabalana, nacuruka, nakhala nazo mphamvu zazikuru; ndipo dziko linadzala nao.

8. Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Aigupto, imene siinadziwa Yosefe.

9. Ndipo ananena ndi anthu ace, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israyeli, acuruka, natiposa mphamvu.

10. Tiyeni, tiwacenjerere angacuruke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kucoka m'dzikomo.

11. Potero anawaikira akuru a misonkho kuti awasautse ndi akatunduno. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo cuma, ndiyo Pitomu ndi Ramese.

12. Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anacuruka, momwemonso anafalikira. Ndipo anabvutika cifukwa ca ana a Israyeli.

13. Ndipo Aaigupto anawagwiritsa ana a Israyeli nchito yosautsa;

14. nawawitsa moyo wao ndi nchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi nchito zonse za pabwalo, nchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.

15. Ndipo mfumu ya Aigupto inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lace la wina ndiye Sifra, dzina la mnzace ndiye Puwa;

16. ninati, Pamene muciza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.

17. Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanacita monga mfumu ya Aigupto inawauza, koma analeka ana amuna akhale ndi moyo.

18. Ndipo mfumu ya Aigupto inaitana anamwino, ninena nao, Mwacita ici cifukwa ninji, ndi kuleka ana amunawo akhale ndi moyo?

19. Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aigupto; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanalike anamwino.

20. Potero Mulungu anawacitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anacuruka, nakhala nazo mphamvu zazikuru.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 1