Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 1:3-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini;

4. Dani ndi Nafitali, Gadi ndi Aseri.

5. Ndipo amoyo onse amene anaturuka m'cuunomwace mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; kama Yosefe anali m'Aigupto.

6. Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ace onse, ndi mbadwo uwo wonse.

7. Ana a Israyeli ndipo anaswana, nabalana, nacuruka, nakhala nazo mphamvu zazikuru; ndipo dziko linadzala nao.

8. Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Aigupto, imene siinadziwa Yosefe.

9. Ndipo ananena ndi anthu ace, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israyeli, acuruka, natiposa mphamvu.

10. Tiyeni, tiwacenjerere angacuruke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kucoka m'dzikomo.

11. Potero anawaikira akuru a misonkho kuti awasautse ndi akatunduno. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo cuma, ndiyo Pitomu ndi Ramese.

12. Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anacuruka, momwemonso anafalikira. Ndipo anabvutika cifukwa ca ana a Israyeli.

13. Ndipo Aaigupto anawagwiritsa ana a Israyeli nchito yosautsa;

14. nawawitsa moyo wao ndi nchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi nchito zonse za pabwalo, nchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 1