Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 1:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. NDIPO maina a ana a Israyeli, amene analowa m'Aigupto ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lace:

2. Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda;

3. Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini;

4. Dani ndi Nafitali, Gadi ndi Aseri.

5. Ndipo amoyo onse amene anaturuka m'cuunomwace mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; kama Yosefe anali m'Aigupto.

6. Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ace onse, ndi mbadwo uwo wonse.

7. Ana a Israyeli ndipo anaswana, nabalana, nacuruka, nakhala nazo mphamvu zazikuru; ndipo dziko linadzala nao.

8. Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Aigupto, imene siinadziwa Yosefe.

9. Ndipo ananena ndi anthu ace, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israyeli, acuruka, natiposa mphamvu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 1