Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 8:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yace nja citsulo, ndi m'mapiri ace mukumbe mkuwa.

10. Ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kuyamika Yehova Mulungu wanu cifukwa ca dziko lokomali anakupatsani.

11. Cenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino;

12. kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo;

13. ndipo zitacuruka ng'ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitacurukanso siliva wanu ndi golidi wanu, zitacurukanso zonse muli nazo;

14. mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo;

15. amene anakutsogolerani m'cipululu cacikuru ndi coopsaco, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakuturutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;

16. amene anakudyetsani m'cipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwa; kuti akucepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akucitireni cokoma potsiriza panu;

17. ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira cuma ici.

18. Koma mukumbukile Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera cuma; kuti akhazikitse cipangano cace cimene analumbirira makolo anu, monga cikhala lero lino.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 8