Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 8:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Cenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino;

12. kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo;

13. ndipo zitacuruka ng'ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitacurukanso siliva wanu ndi golidi wanu, zitacurukanso zonse muli nazo;

14. mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo;

15. amene anakutsogolerani m'cipululu cacikuru ndi coopsaco, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakuturutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;

16. amene anakudyetsani m'cipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwa; kuti akucepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akucitireni cokoma potsiriza panu;

17. ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira cuma ici.

18. Koma mukumbukile Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera cuma; kuti akhazikitse cipangano cace cimene analumbirira makolo anu, monga cikhala lero lino.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 8