Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 6:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.

10. Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikuru ndi yokoma, imene simunaimanga;

11. ndi nyumba zodzala nazo zokoma ziri zonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda yaazitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta;

12. pamenepo mudzicenjere mungaiwale Yehova, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo,

13. Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzichula dzina lace.

14. Musamatsata milungu yina, milungu yina ya mitundu ya anthu akuzinga inu;

15. pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukucotsani pankhope pa dziko lapansi.

16. Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa m'Masa.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 6