Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 6:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. pamenepo mudzicenjere mungaiwale Yehova, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo,

13. Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzichula dzina lace.

14. Musamatsata milungu yina, milungu yina ya mitundu ya anthu akuzinga inu;

15. pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukucotsani pankhope pa dziko lapansi.

16. Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa m'Masa.

17. Muzisunga mwacangu malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi mboni zace, ndi malemba ace, amene anakulamulirani.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 6