Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 5:6-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakuturutsa m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo.

7. Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.

8. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko;

9. usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana cifukwa ca atate wao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai wa iwo amene akudana ndi Ine;

10. ndi kucitira cifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga.

11. Usaehuledzinala Yehova Mulungu wako pacabe; cifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosacimwa amene achula pacabe dzina lacelo.

12. Samalira tsiku la Sabata likhale lopatulika, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira.

13. Masiku asanu ndi limodzi uzigwiritsa nchito, ndi kucita nchito zako zonse;

14. koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira nchito iri yonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wanchito wako wamwamuna, kapena wanchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena buru wako, kapena zoweta zako ziri zonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wanchito wako wamwamuna ndi wanchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.

15. Ndipo uzikumbukilakuti unali kapolo m'dziko la Aigupto, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakuturutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; cifukwa cace Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.

16. Lemekeza atate wako ndi amako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako acuruke, ndi kuti cikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

17. Usaphe.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 5