Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 5:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mose anaitana Israyeli wonse, nanena nao, Tamverani, Israyeli, malemba ndi maweruzo ndinenawa m'makutu mwanu lero, kuti muwaphunzire, ndi kusamalira kuwacita.

2. Yehova Mulungu wathu anapangana nafe cipangano m'Horebe.

3. Yehova sanacita cipangano ici ndi makolo athu, koma ndi ife, ife amene tiri ndi moyo tonsefe pane lero.

4. Yehova ananena ndi inu popenyana maso m'phirimo, ali pakati pa moto,

5. (ndinalinkufma pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munacita mantha cifukwa ca moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti:

6. Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakuturutsa m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo.

7. Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.

8. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko;

9. usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana cifukwa ca atate wao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai wa iwo amene akudana ndi Ine;

10. ndi kucitira cifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 5