Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 4:42-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wace dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa midzi iyi, akhale ndi moyo:

43. ndiyo Bezere, m'cipululu, m'dziko lacidikha, ndiwo wa Anrubeni; ndi Ramoti m'Gileadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, m'Basana, ndiwo wa Amanase.

44. Ndipo ici ndi cilamulo Mose anaciika pamaso pa ana a Israyeli;

45. izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israyeli, poturuka iwo m'Aigupto;

46. tsidya lija la Yordano, m'cigwa ca pandunji pa Beti Peori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israyeli anamkantha, poturuka iwo m'Aigupto;

47. ndipo analanda dziko lace, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basana, mafumu awiri a Aamori, akukhala tsidya lija la Yordano loturuka dzuwa;

48. kuyambira ku Aroeri, ndiwo m'mphepete mwa mtsinje wa Arinoni, kufikira phiri la Sioni (ndilo Herimoni),

49. ndi cidikha conse tsidya lija la Yordana kum'mawa, kufikira nyanja ya kucidikha, pa tsinde lace la Pisiga.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 4