Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 4:41-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Pamenepo Mose anapatula midzi itatu tsidya lija la Yordano loturuka dzuwa;

42. kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wace dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa midzi iyi, akhale ndi moyo:

43. ndiyo Bezere, m'cipululu, m'dziko lacidikha, ndiwo wa Anrubeni; ndi Ramoti m'Gileadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, m'Basana, ndiwo wa Amanase.

44. Ndipo ici ndi cilamulo Mose anaciika pamaso pa ana a Israyeli;

45. izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israyeli, poturuka iwo m'Aigupto;

46. tsidya lija la Yordano, m'cigwa ca pandunji pa Beti Peori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israyeli anamkantha, poturuka iwo m'Aigupto;

47. ndipo analanda dziko lace, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basana, mafumu awiri a Aamori, akukhala tsidya lija la Yordano loturuka dzuwa;

48. kuyambira ku Aroeri, ndiwo m'mphepete mwa mtsinje wa Arinoni, kufikira phiri la Sioni (ndilo Herimoni),

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 4