Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 4:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo tsopano, Israyeli, dioloketu tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwacite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani.

2. Musamaonjeza pa mau amene ndikuuzani, kapena kucotsapo, kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani.

3. Maso anu anapenya cocita Yehova cifuwa ca Baala Peori; pakuti amuna onse amene anatsata Baala Peori, Yehova Mulungu wanu anawaononga pakati panu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 4