7. Kumbukirani masiku akale,Zindikirani zaka za mibadwo yambiri;Funsani atate wanu, adzakufotokozerani;Akuru anu, adzakuuzani.
8. Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu colowacao,Pamene anagawa ana a anthu,Anaika malire a mitundu ya anthu,Monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israyeli,
9. Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ace;Yakobo ndiye muyeso wa colowacace.
10. Anampeza m'dziko la mabwinja, ndi m'cipululu colira copanda kanthu;Anamzinga, anamlangiza,Anamsunga ngati kamwana lea m'diso;