Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 32:5-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Anamcitira zobvunda si ndiwo ana ace, cirema ncao;Iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.

6. Kodi mubwezera Yehova cotero,Anthu inu opusa ndi opanda nzeru?Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuyewanu;Anakulengani, nakukhazikitsani?

7. Kumbukirani masiku akale,Zindikirani zaka za mibadwo yambiri;Funsani atate wanu, adzakufotokozerani;Akuru anu, adzakuuzani.

8. Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu colowacao,Pamene anagawa ana a anthu,Anaika malire a mitundu ya anthu,Monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israyeli,

9. Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ace;Yakobo ndiye muyeso wa colowacace.

10. Anampeza m'dziko la mabwinja, ndi m'cipululu colira copanda kanthu;Anamzinga, anamlangiza,Anamsunga ngati kamwana lea m'diso;

11. Monga mphungu ikasula cisa cace,Nikapakapa pa ana ace,Iye anayala mapiko ace, nawalandira,Nawanyamula pa mapiko ace;

12. Yehova yekha anamtsogolera,Ndipo palibe mulungu wacilendo naye.

13. Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi,Ndipo anadya zipatso za m'minda;Namyamwitsa uci wa m'thanthwe,Ndi mafutam'mwala wansangalabwe;

14. Mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa,Ndi mafuta a ana a nkhosa,Ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basana, ndi atonde,Ndi imso zonenepa zatirigu;Ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa,

15. Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira;Wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta;Pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga,Napeputsa thanthwe la cipulumutso cace.

16. Anamcititsa nsanje ndi milungu yacilendo,Anautsa mkwiyo wace ndi zonyansa.

17. Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai;Milungu yosadziwa iwo,Yatsopano yofuma pafupi, Imene makolo anu sanaiopa,

18. Mwaleka Thanthwe limene linakubalani,Mwaiwala Mulungu amene anakulengani.

19. Ndipo Yehova anaciona, nawanyoza,Pakuipidwa nao ana ace amuna, ndi akazi.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 32