Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 32:44-52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

44. Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m'makutu mwa anthu, iye, ndi Hoseya mwana wa Nuni.

45. Ndipo Mose anatha kunena mau awa onse kwa Israyeli wonse;

46. nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikucitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwacita mau onse a cilamulo ici.

47. Pakuti sicikhala kwa inu cinthu copanda pace, popeza ndico moyo wanu, ndipo mwa cinthu ici mudzacurukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordano, kulilandira.

48. Ndipo Yehova ananena ndi Mose tsiku lomweli, ndi kuti,

49. Kwera m'phiri muno mwa Abarimu, phiri la Nebo, lokhala m'dziko la Moabu, popenyana ndi Yeriko; nupenye dziko la Kanani, limene ndipereka kwa ana a Israyeli likhale lao lao;

50. nufe m'phiri m'mene ukweramo, nuitanidwe kumka kwa anthu a mtundu wako; monga Aroni mbale wako anafa m'phiri la Hori, naitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wace;

51. popeza munandilakwira pakati pa ana a Israyeli ku madzi a Meriba wa Kadesi m'cipululu ca Zini, popeza simunandipatula Ine pakati pa ana a Israyeli,

52. Pakuti udzapenya dzikoli pandunji pako; koma osalowako ku dziko limene ndipatsa ana a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 32