Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 32:16-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Anamcititsa nsanje ndi milungu yacilendo,Anautsa mkwiyo wace ndi zonyansa.

17. Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai;Milungu yosadziwa iwo,Yatsopano yofuma pafupi, Imene makolo anu sanaiopa,

18. Mwaleka Thanthwe limene linakubalani,Mwaiwala Mulungu amene anakulengani.

19. Ndipo Yehova anaciona, nawanyoza,Pakuipidwa nao ana ace amuna, ndi akazi.

20. Ndipo iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga,Ndidzaona kutsiriza kwao;Popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira,Ana osakhulupirika iwo.

21. Anautsa nsanje yanga ndi cinthu cosati Mulungu;Anautsa mkwiyo wanga om zopanda pace zao.Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu;Ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa.

22. Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga,Utentha kumanda kunsiUkutha dziko lapansi ndi zipatso zaceNuyatsa maziko a mapiri,

23. Ndidzawaunjikira zoipa;Ndidzawathera nubvi yanga.

24. Adzaonda nayo njalaAdzanyekeka ndi makala a moto, cionongeko cowawa;Ndipo ndidzawatumizira mana a zirombo,Ndi ululu wa zokwawa m'pfumbi.

25. Pabwalo lupanga lidzalanda,Ndi m'zipinda mantha;Lidzaononga mnyamata ndi namwali,Woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi.

26. Ndinati, Ndikadawauzira ndithu,Ndikadafafaniza cikumbukiro cao mwa anthu;

27. Ndikadapanda kuopa mkwiyo wapamdani,Angayese molakwa outsana nao,Anganene, Lakwezeka dzanja lathu,Ndipo Yehova sanacita ici conse.

28. Popeza iwo ndiwo mtundu wa anthu wosowa uphungu konse,Ndipo alibe cidziwitso.

29. Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ici,Akadasamalira citsirizo cao!

30. Mmodzi akadapitikitsa zikwi,Awiri akadathawitsa zikwi khumi,Akadapanda kuwagulitsa Thanthwelao,Akadapanda kuwapereka Yehova.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 32