Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 32:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa,Ndi mafuta a ana a nkhosa,Ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basana, ndi atonde,Ndi imso zonenepa zatirigu;Ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa,

15. Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira;Wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta;Pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga,Napeputsa thanthwe la cipulumutso cace.

16. Anamcititsa nsanje ndi milungu yacilendo,Anautsa mkwiyo wace ndi zonyansa.

17. Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai;Milungu yosadziwa iwo,Yatsopano yofuma pafupi, Imene makolo anu sanaiopa,

18. Mwaleka Thanthwe limene linakubalani,Mwaiwala Mulungu amene anakulengani.

19. Ndipo Yehova anaciona, nawanyoza,Pakuipidwa nao ana ace amuna, ndi akazi.

20. Ndipo iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga,Ndidzaona kutsiriza kwao;Popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira,Ana osakhulupirika iwo.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 32