Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 32:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kumwamba kuchere khutu, ndipo ndidzanena;Ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga;

2. Ciphunzitso canga cikhale ngati mvula;Maneno anga agwe ngati mame;Ngati mvula yowaza pamsipu,Ndi monga madontho a mvula pazitsamba.

3. Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova;Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu.

4. Thanthwe, nchito yace ndi yangwiro;Pakuti njira zace zonse ndi ciweruzo;Mulungu wokhulupirika ndi wopanda cisalungamo;Iye ndiye wolungama ndi wolunjika,

5. Anamcitira zobvunda si ndiwo ana ace, cirema ncao;Iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.

6. Kodi mubwezera Yehova cotero,Anthu inu opusa ndi opanda nzeru?Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuyewanu;Anakulengani, nakukhazikitsani?

7. Kumbukirani masiku akale,Zindikirani zaka za mibadwo yambiri;Funsani atate wanu, adzakufotokozerani;Akuru anu, adzakuuzani.

8. Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu colowacao,Pamene anagawa ana a anthu,Anaika malire a mitundu ya anthu,Monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israyeli,

9. Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ace;Yakobo ndiye muyeso wa colowacace.

10. Anampeza m'dziko la mabwinja, ndi m'cipululu colira copanda kanthu;Anamzinga, anamlangiza,Anamsunga ngati kamwana lea m'diso;

11. Monga mphungu ikasula cisa cace,Nikapakapa pa ana ace,Iye anayala mapiko ace, nawalandira,Nawanyamula pa mapiko ace;

12. Yehova yekha anamtsogolera,Ndipo palibe mulungu wacilendo naye.

13. Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi,Ndipo anadya zipatso za m'minda;Namyamwitsa uci wa m'thanthwe,Ndi mafutam'mwala wansangalabwe;

14. Mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa,Ndi mafuta a ana a nkhosa,Ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basana, ndi atonde,Ndi imso zonenepa zatirigu;Ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa,

15. Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira;Wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta;Pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga,Napeputsa thanthwe la cipulumutso cace.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 32