Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:39-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Mudzanka m'minda yamphesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wace, kapena kuchera mphesa zace, popeza citsenda cidzaidya.

40. Mudzakhala nayo mitengo yaazitona m'malire anu onset osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo yaazitona zidzapululuka.

41. Mudzabala ana amuna ndi akazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo.

42. Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zao zao za dzombe.

43. Mlendo wokhala pakati panu adzakulira-kulira inu, koma inu mudzacepera-cepera.

44. Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mcira.

45. Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ace ndi malemba ace amene anakulamulirani;

46. ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati cizindikilo ndi cozizwa, nthawi zonse.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28