Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:34-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. nimudzakhala oyeruka cifukwa comwe muciona ndi maso anu,

35. Yehova adzakukanthani ndi cironda coipa cosacira naco kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pa mutu panu.

36. Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu yina ya mitengo ndi miyala.

37. Ndipo mudzakhala codabwitsa, ndi nkhani, ndi nthanthi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko.

38. Mudzaturuka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.

39. Mudzanka m'minda yamphesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wace, kapena kuchera mphesa zace, popeza citsenda cidzaidya.

40. Mudzakhala nayo mitengo yaazitona m'malire anu onset osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo yaazitona zidzapululuka.

41. Mudzabala ana amuna ndi akazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo.

42. Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zao zao za dzombe.

43. Mlendo wokhala pakati panu adzakulira-kulira inu, koma inu mudzacepera-cepera.

44. Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mcira.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28