Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 27:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo ayankhe Alevi ndi kunena kwa amuna onse a Israyeli, ndi mau omveka.

15. Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, nchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse: ayankhe ndi kuti, Amen.

16. Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wace kapena mai wace. Ndi anthu onse anene, Amen.

17. Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wace. Ndi anthu onse anene, Amen.

18. Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m'njira, Ndi anthu onse anene, Amen.

19. Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.

20. Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wace; popeza wabvula atate wace. Ndi anthu onse anene, Amen.

21. Wotembereredwa iye wakugona ndi nyama iri yonse. Ndi anthu onse anene, Amen.

22. Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wace, mwana wamkazi wa atate wace, kapena mwana wamkazi wa mace. Ndi anthu onae anene, Amen.

23. Wotembereredwa iye wakugona ndi mpongozi wace. Ndi anthu onse anene, Amen.

24. Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wace m'tseri. Ndi anthu onse anene, Amen.

25. Wotembereredwa iye wakulandira camwazi cakuti akanthe munthu wosacimwa. Ndi anthu onse anene, Amen.

26. Wotembereredwa iye wosabvomereza mau a cilamulo ici kuwacita. Ndi anthu onse anene, Amen.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 27