Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 27:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Aimirire awa pa phiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordano: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.

13. Naimirire awa pa phiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Aseri, ndi Zebuloni, Dani, ndi Nafitali.

14. Ndipo ayankhe Alevi ndi kunena kwa amuna onse a Israyeli, ndi mau omveka.

15. Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, nchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse: ayankhe ndi kuti, Amen.

16. Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wace kapena mai wace. Ndi anthu onse anene, Amen.

17. Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wace. Ndi anthu onse anene, Amen.

18. Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m'njira, Ndi anthu onse anene, Amen.

19. Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.

20. Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wace; popeza wabvula atate wace. Ndi anthu onse anene, Amen.

21. Wotembereredwa iye wakugona ndi nyama iri yonse. Ndi anthu onse anene, Amen.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 27