Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 26:17-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m'njira zace, ndi kusunga malemba ace, ndi malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi kumvera mau ace.

18. Ndipo Yehova wakulonjezetsani lero kuti mudzakhala anthu ace ace a pa okha, monga ananena ndi inu, ndi kuti mudzasunga malamulo ace onse;

19. kuti akukulitseni koposa amitundu onse anawalenga, wolemekezeka, womveka dzina, ndi waulemu; ndi kuti mukhale mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu wanu monga ananena.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 26