Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 25:14-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Musamakhala nayo m'nyumba yanu miyeso ya efa yosiyana, waukuru ndi waung'ono.

15. Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu acuruke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

16. Pakuti onse akucita zinthu izi, onse akucita cisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 25